Chichewa Hymn

Bwenzi Lathu Ndiye Yesu


1.Bwenzi lathu ndiye Yesu, Atikonda ifetu,
Zifunsiro zathu zonse, Tipemphere Mbuyathu;
Mtima phe tisowa tonse, Zitibvuta cabeko,
Kaamba sitimanka konse Kumpemphera Mlunguyo.


2.Tiri nazo zotiyesa, Zitidetsa nkhawamu,
Tisadandaule cabe, Timpephere Mbuyathu;
Kodi tikaona wina, Timkhulupiramo?
Yesu atidziwa bwino, Timpemphere yekhayo.


3.Kodi titolema namo, Zotiwawa m’mitmamo,
Atipulumutsa Yesu, TImpempere Iyeyu.
Kodi atothawa ’bale, Pempheratu bwenzilo,
Akusunga mkono mwace, Udzapumuliramo.

 


Chisomo chodabwitsacho


Chisomo chodabwitsacho,
Chapulumutsa ‘ne;
Woipa wopambanatu,
Ndapeza moyo ‘ne.


Chisomocho chachotsadi
Mantha a imfayo
Pakukhulupirira ‘Ye,
Ambuye Yesuyo.


Chisomo chandisungadi,
Panjira yangayo,
Chisomo chidzasunga ‘ne
Mpakatu kwathuko.


Kwathu ndidzaimba nyimbo
Ya chisomo chake,
Yolemekeza Mlunguyo
Kunthawi zosatha.

 


Cholimbitsa mtima