Tiyeni Akhristu
Usikuwo woyerawo
1. Usikuwo woyerawo!
Mwana adamlerayo
Akakhale Mfumuyo,
Anabadwa m’kholamo,
Mfumu ya mafumu
Ndi ya anthuwo.
2. Mwanayo wa Mulunguyo
Andikonda inetu,
Nan’tayira chumacho
Nadzagona m’udzumo
Ndiyamika Mbuye
Wanga Yesuyo.
3. Usikuwo woyerawo!
Wadzatu mtenderewo;
Ife tonse anthuwo
Atitenga Mlunguyo
Mlemkeze ‘Tate
Mwana, Mzimunso
Werenga Madalitso ako
Pamene zovuta za dziko zazinga
Pamene wakhumudwa zonse zataika
Werenga zabwino zomwe uli nazo
Ndipo udzazindikira mbuye ngokoma
Ref
Werenga Madalitso ako, Utchule limodzi limodzi,
Werenga Madalitso ako, Ona zimene Mulungu wakuchitira
Kodi walemedwa ndi zovuta zadziko
Kapena mtanda wako ukulemera
Werenga zabwino zomwe uli nazo
Ndipo udzaimba nyimbo yomutamanda
Tsopano pakati pamavuto ako
Usataye mtima Mulungu akuona
Ganiza zabwino zomwe wakuchitira
Adzakugwira dzanja ulendo onsewo
https://youtu.be/eQFfdCLUohc