Pokhala Mtendere
Pakwitana Mbuye Wanga
1. Pakwitana Mbuye wanga
Potsiriza dzikoli,
Pakufika tsiku lakuwalalo
Posonkhana akumvera,
Pakuona Yesuyo,
Tidzakondwerera naye komweko.
Refrain
Pakwitana Mbuye wanga,
Pakwitana Mbuye wanga,
Pakwitana Mbuye wanga,
Tidzakondwerera naye komweko.
2. Potuluka m’manda mwawo
Anthu ake onsewo,
Tidzasanganatu naow nthawiyo,
Pakuuka osankhidwa,
Kunka naye Yesuyo,
Ndidzakondwerera naye komweko.
3. Tisaleke kigwirabe
Ntchito ya Mulunguyo,
Tibukitse mbiri yake m’dzikoli,
Ndi podzatha moyo wathu
Ndi zintchito zathuzo,
Tidzakonddwerera naye komweko.
Tamani mphamvu
1. Tamani mphamvu ya Yesu,
Angelo agwade;
Tulutsani korona,
Ref
Mubveke, mbveke, mbveke,
Mbveke, Mbuyeyo!
2. Inu osankhidwa ake,
Owomboledwa ‘nu,
Tamani Mpulumutsiyo,
3. Anthu ose ndi mitundu
Pa dziko linotu,
Amlemekeze Mfumuyi,
4. Tifuna kuti komweko
Tikamgwadire ‘Ye;
Tidzaimba kosaleka;